NSANJA YA OLONDA

Funso: Kwa zaka zambiri, anthu ena akhala akuchita zinthu zosiyanasiyana kuti Baibulo lisapezekenso, koma mpaka pano lidakalipobe. Kodi umenewu si umboni wokwanira woti linachokeradi kwa Mulungu?

Lemba: Yes. 40:8

Perekani Magaziniyo: Nkhani zomwe zili m’magaziniyi zikufotokoza zimene anthu akhala akuchita pofuna kuti Baibulo lisapezekenso.

NSANJA YA OLONDA (tsamba lomaliza)

Funso: Ndikufuna kumva maganizo anu pa funso ili. [Werengani funso loyamba patsamba 16.] Anthu ena amakhulupirira kuti anthu ndi amene anayambitsa zipembedzo. Koma ena amaganiza kuti Mulungu ndi amene anayambitsa chipembedzo kuti anthu azimulambira. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Lemba: Yak. 1:27

Perekani Magaziniyo: Nkhaniyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi. Ndidzabweranso kuti tidzakambirane mfundo zina za m’nkhaniyi.

UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU

Funso: Nkhani zimene anthu amawerenga m’nyuzipepala masiku ano ndi zimene Baibulo linaneneratu. Kodi ndi zinthu ziti zimene Baibulo linaneneratu zomwe inuyo munamva kapena kuona zikuchitika?

Lemba: 2 Tim. 3:1-5

Perekani Kabukuko: Kabukuka kakufotokoza kuti anthu amene amakonda Mulungu amaona kuti zikuchitikazi ndi chizindikiro choti tili m’masiku otsiriza. [Muonetseni funso lachiwiri pamutu woyamba.]

LEMBANI ULALIKI WANUWANU

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.