Masiku ano pali zinthu zambiri zomwe zingatilepheretse kuchita zinthu zofunika. Mwachitsanzo, pamafunika nthawi komanso mphamvu kuti munthu apite kukagula zinthu, alipire zimene wagula, akonzetse komanso kuteteza zinthuzo kuti ena asamubere. Yesu ankakhala moyo wosalira zambiri chifukwa sankafuna kuti zinthu zina zimulepheretse kuchita utumiki wake.Mat. 8:20.

Kodi ndi zinthu ziti zimene mukufuna kusintha pa moyo wanu kuti muzichita zambiri mu utumiki? Kodi mungasinthe zinthu zina ndi zina kuti munthu wina wa m’banja lanu ayambe upainiya? Ngati panopa mumachita kale utumiki wa nthawi zonse, kodi mwayamba kulola kuti zinthu zina zikulepheretseni kuchita zinthu zofunika kwambiri? Munthu amene amatumikira Yehova amasangalala kwambiri ngati amakhala moyo wosalira zambiri.1 Tim. 6:7-9.

Lembani zimene mungachite kuti muzikhala moyo wosalira zambiri.