Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 74-78

Tiziganizira Zinthu Zabwino Zimene Yehova Wachita

Tiziganizira Zinthu Zabwino Zimene Yehova Wachita

Tiziganizira zinthu zabwino zimene Yehova wachita

74:16; 77:6, 11, 12

 • Tikamaganizira zimene tikuphunzira m’Mawu a Mulungu timamvetsa zimene tikuwerengazo komanso timayamba kuona kufunika kwa zimene Yehova amatiphunzitsa

 • Kuganizira mozama zokhudza Yehova kumatithandiza kuti tizikumbukira ntchito zodabwitsa zimene anachita komanso zimene walonjeza kuti adzachita m’tsogolo

Ntchito za Yehova ndi monga izi:

74:16, 17; 75:6, 7; 78:11-17

 • Kulenga

  Tikamaphunzira zambiri zokhudza chilengedwe m’pamenenso timagoma ndi ntchito za Yehova

 • Kusankha amuna oti azitsogolera mumpingo

  Tiyenera kumagonjera anthu amene Yehova wawasankha kuti azititsogolera

 • Kuteteza atumiki ake

  Kukumbukira kuti Yehova amateteza atumiki ake kumatithandiza kuti tizimudalira kwambiri komanso kuti tisamakayikire kuti adzatiteteza