Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 69-73

Anthu a Mulungu ndi Odzipereka Potumikira Yehova

Anthu a Mulungu ndi Odzipereka Potumikira Yehova

Tiyenera kumachita zinthu zosonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu

69:9

  • Pa moyo wake wonse, Davide anali wodzipereka kwambiri potumikira Yehova

  • Davide sankalola kuti anthu azinyoza dzina la Yehova

Akhristu achikulire angathandize achinyamata kukhala odzipereka

71:17, 18

  • Munthu amene analemba Salimo limeneli, yemwe mwina ndi Davide, ankafunitsitsa kudzalimbikitsa m’badwo wa m’tsogolo

  • Makolo komanso Akhristu odziwa zambiri, angathandize achinyamata kuti azikonda Yehova

Tikakhala odzipereka timafunitsitsa kuuza ena zimene Ufumu wa Mulungu udzatichitire

72:3, 12, 14, 16-19

  • Vesi 3—Aliyense adzakhala pamtendere

  • Vesi 12—Mulungu adzalanditsa anthu osauka

  • Vesi 14—Sikudzakhalanso anthu achiwawa

  • Vesi 16—Kudzakhala chakudya cha mwana alirenji