Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu–Ndandanda ya Misonkhano  |  July 2016

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mungachite Upainiya kwa Chaka Chimodzi?

Kodi Mungachite Upainiya kwa Chaka Chimodzi?

Kodi mungapeze madalitso otani ngati mutachita upainiya?Miy. 10:22.

MUKAMACHITA UPAINIYA, MUKHOZA KUPEZA MADALITSO OTSATIRAWA:

  • Mukhoza kukhala ndi luso lolalikira ndipo mungamasangalale mu utumiki.

  • Mungamakonde kwambiri Yehova. Mukamauza ena zokhudza Yehova m’pamenenso mumaganizira kwambiri za makhalidwe ake abwino.

  • Mungaone ubwino woika zinthu za Ufumu pamalo oyamba m’malo mwa zofuna zanu. Mungakhalenso osangalala mukamagwiritsa ntchito nthawi komanso zinthu zanu pothandiza ena mu utumiki.Mat. 6:33; Mac. 20:35

  • Mukhoza kulowa Sukulu ya Apainiya, kuchita nawo msonkhano wa apainiya womwe umachitika msonkhano wadera ukayandikira komanso womwe woyang’anira dera amachititsa akamachezera mpingo.

  • Mungapeze anthu ambiri oti muziphunzira nawo Baibulo.

  • Mungamakhale nthawi yaitali muli ndi abale ndi alongo, omwe angakulimbikitseni komanso kukuthandizani.Aroma 1:11, 12