Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU–NDANDANDA YA MISONKHANO JULY 2016

July 25-31

MASALIMO 79-86

July 25-31

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Kodi Munthu Wofunika Kwambiri pa Moyo Wanu ndi Ndani?”: (10 min.)

  • Sal. 83:1-5—Cholinga chathu chachikulu chizikhala kulemekeza dzina la Yehova komanso ulamuliro wake (w08 10/15 13 ndime 7-8)

  • Sal. 83:16—Tikamakhalabe okhulupirika ngakhale pamavuto, dzina la Yehova limalemekezedwa (w08 10/15 15 ndime 16)

  • Sal. 83:17, 18—Yehova ndi wofunika kwambiri m’chilengedwe chonse (w11 5/15 16 ndime 1-2; w08 10/15 15-16 ndime 17-18)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Sal. 79:9—Kodi lemba limeneli lingatithandize bwanji kudziwa zimene tinganene m’mapemphero athu? (w06 7/15 12 ndime 5)

  • Sal. 86:5—Kodi Yehova ndi “wokonzeka kukhululuka” motani? (w06 7/15 12 ndime 9)

  • Kodi ndaphunzira chiyani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Sal. 85:8–86:17

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 111

 • Kodi Mulungu Ali Ndi Dzina?: (15 min.) Yambani ndi kuonera vidiyo yakuti Kodi Mulungu Ali Ndi Dzina? (Kuti mupeze vidiyoyi, pitani pamene palembedwa kuti, MABUKU > MAVIDIYO. Kenako pitani pomwe pali kabuku ka Uthenga Wabwino. Vidiyoyi ikupezeka paphunziro 2 lakuti “Kodi Mulungu Ndani?”) Kenako kambiranani mafunso otsatirawa: Kodi tingagwiritse ntchito bwanji vidiyoyi tikamalalikira mwamwayi, pamalo opezeka anthu ambiri komanso tikamalalikira kunyumba ndi nyumba? Kodi ndi zosangalatsa zotani zimene zinakuchitikirani pamene munkagwiritsa ntchito vidiyoyi?

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 3 ndime 1-13, bokosi patsamba 29

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 143 ndi Pemphero

  Kumbukirani kuti, muyenera kuika nyimboyi kuti onse amvetsere, kenako muibwerezenso kuti onse aimbe nawo.