Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Akulalikira munthu wothyola tiyi ku Cameroon

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU July 2016

Zitsanzo za Ulaliki

Mfundo zokuthandizani pogawira Nsanja ya Olonda ndi kabuku ka Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mupange ulaliki wanuwanu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Tamandani Yehova Wakumva Pemphero

N’chifukwa chiyani muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni kukwaniritsa zimene munamulonjeza? Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakhulupirira Yehova mukamapemphera? (Masalimo 61-65)

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizikhala Moyo Wosalira Zambiri Kuti Tizitumikira Bwino Mulungu

Kodi kukhala moyo wosalira zambiri kungakuthandizeni kuti muzitha kuchita chiyani? Kodi mungatsanzire bwanji moyo umene Yesu ankakhala?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Anthu a Mulungu ndi Odzipereka Potumikira Yehova

Kodi tikuphunzira chiyani kwa Davide pa nkhani ya kudzipereka kwa Mulungu? Kodi anthu odzipereka kwa Yehova amafunitsitsa kuchita chiyani? (Masalimo 69-72)

MOYO WACHIKHRISTU

Kodi Mungachite Upainiya kwa Chaka Chimodzi?

Anthu amene amasintha zinthu zina pa moyo wawo kuti achite upainiya amakhala osangalala komanso amapeza madalitso ambiri.

MOYO WACHIKHRISTU

Ndandanda ya Upainiya Wokhazikika

Mungadabwe kudziwa kuti ngakhale anthu amene amadwaladwala kapena amene amagwira ntchito akhoza kuchita upainiya wokhazikika.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Tiziganizira Zinthu Zabwino Zimene Yehova Wachita

Kodi ndi zinthu ziti zimene Yehova wakhala akuchita? Kodi kuganizira zimenezi kungatithandize bwanji? (Masalimo 74-78)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Kodi Munthu Wofunika Kwambiri pa Moyo Wanu ndi Ndani?

Munthu amene analemba Salimo 83 anasonyeza kuti Yehova anali wofunika kwambiri pa moyo wake. Kodi nafenso tingatani kuti tizisonyeza kuti Yehova ndi wofunika kwambiri pa moyo wathu?