CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Chifuniro cha Yehova Chichitike”: (10 min.)

  • Mac. 21:8-12​—Akhristu anzake a Paulo anamupempha kuti asapite ku Yerusalemu chifukwa cha mavuto amene ankayembekezera kukakumana nawo kumeneko (bt 177-178 ¶15-16)

  • Mac. 21:13​—Paulo anali wofunitsitsa kuchita zimene Yehova ankafuna (bt 178 ¶17)

  • Mac. 21:14​—Abale ataona kuti Paulo watsimikiza mtima, anasiya kumuletsa (bt 178 ¶18)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Mac. 21:23, 24​—N’chifukwa chiyani akulu a ku Yerusalemu anauza Paulo malangizo amenewa ngakhale kuti pa nthawiyi Akhristu sanalinso pansi pa Chilamulo cha Mose? (bt 184-185 ¶10-12)

  • Mac. 22:16​—Kodi kubatizidwa kwa Paulo kunachotsa bwanji machimo ake? (“kusamba kuti uchotse machimo ako mwa kuitana pa dzina lake” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 22:16, nwtsty)

  • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mac. 21:1-19 (th phunziro 5) *

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

^ ndime 15 ^ ndime 18 Dziwani izi: Kuyambira mwezi uno, Ndandanda ya Utumiki izikhala ndi phunziro limene wophunzira wapatsidwa lomwe lizikhala kutsogolo kwa nkhani yake mumkutira mawu. Phunziroli lizichokera m’kabuku kakuti Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso (th).