27:23, 24; 28:1, 2, 16, 17

Ngakhale kuti Paulo anali atamangidwa, sanasiye kuuza ena zimene ankakhulupirira. Pamene anali mungalawa analalikira kwa oyendetsa komanso anthu ena amene anakwera ngalawayo. N’zosakayikitsa kuti ngalawayo itasweka pachilumba cha Melita, iye anapeza mwayi wouza uthenga wabwino anthu amene anawachiritsa. Patangodutsa masiku atatu atafika ku Roma, anasonkhanitsa akuluakulu a Ayuda kuti awalalikire. Komanso pa zaka ziwiri zomwe anali pa ukaidi wosachoka panyumba, ankalalikira kwa anthu amene ankabwera kudzamuona.

Kodi mungatani kuti muzilalikira uthenga wabwino ngakhale kuti mukukumana ndi mavuto osiyanasiyana?