CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Yesu Ankakonda Anthu”: (10 min.)

  • Mat. 8:1-3​—Yesu anachitira chifundo munthu wodwala khate (“kumukhudza” ”Ndikufuna” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 8:3, nwtsty)

  • Mat. 9:9-13​—Yesu ankakonda anthu omwe ankanyozedwa ndi ena (“kudya patebulo” “okhometsa msonkho” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 9:10, nwtsty)

  • Mat. 9:35-38​—Kukonda anthu kunachititsa kuti Yesu azilalikira uthenga wabwino ngakhale atatopa ndiponso anapempha Mulungu kuti atumize antchito ambiri oti agwire ntchitoyi (“anawamvera chisoni” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 9:36, nwtsty)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Mat. 8:8-10​—Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Yesu anakambirana ndi mkulu wa asilikali? (w02 8/15 13 ¶16)

  • Mat. 9:16, 17​—Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pofotokoza mafanizo awiriwa? (jy 70 ¶6)

  • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mat. 8:1-17

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha zimene tinganene. Muitanireni ku misonkhano yathu.

 • Ulendo Wobwereza Wachitatu: (Osapitirira 3 min.) Sankhani lemba komanso buku limene mukufuna kugwiritsa ntchito.

 • Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) bhs 47 ¶18-19

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 145

 • ‘Mulungu Anamuika Kukhala Ambuye ndi Khristu’​—Mbali Yoyamba​—Mbali ina ya vidiyoyi: (15 min.) Nkhani yokambirana. Werengani Mateyu 9:18-25, kenako onerani mbali ya vidiyoyi. Mukamaliza kambiranani mafunso otsatirawa:

  • Kodi Yesu anasonyeza bwanji chifundo kwa Yairo komanso mzimayi wina yemwe ankadwala?

  • Kodi nkhaniyi yakuthandizani bwanji kukhulupirira maulosi a m’Baibulo onena zimene zidzachitike Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira?

  • Kodi tingatsanzire Yesu pa nkhani yokonda anthu m’njira zina ziti?

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 13 ¶11-23

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 95 ndi Pemphero