3:4

  • Zovala za Yohane zinkasonyezeratu kuti ankakhala moyo wosalira zambiri komanso kuti anali wodzipereka pochita chifuniro cha Mulungu

  • Yohane anali ndi mwayi wapadera kwambiri wogwira ntchito yodziwitsa anthu za kubwera kwa Yesu

Kukhala ndi moyo wosalira zambiri kungatithandize kuti tizichita zochuluka potumikira Mulungu ndipo tingamakhale osangalala. Kuti tikhale ndi moyo wosalira zambiri tiyenera . . .

  • kuzindikira zinthu zomwe ndi zofunikadi

  • kusiya kugula zinthu zosafunika kwenikweni

  • kulemba bajeti

  • kuchotsa zinthu zimene sitizigwiritsa ntchito

  • kulipira ngongole zonse

  • kuchepetsa nthawi imene timagwira ntchito

Yohane ankangodya dzombe ndi uchi

Kodi ndingakwaniritse cholinga chiti ngati nditamakhala moyo wosalira zambiri?