CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Ufumu Wakumwamba Wayandikira”: (10 Min.)

  • [Onetsani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Mateyu.]

  • Mat. 3:1, 2​—Yohane M’batizi ankalalikira kuti Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kufika (“kulalikira” “ufumu” “ufumu wakumwamba” “wayandikira” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 3:1, 2, nwtsty)

  • Mat. 3:4​—Yohane M’batizi ankakhala moyo wosalira zambiri ndipo ankadzipereka ndi mtima wonse pochita chifuniro cha Mulungu (“Zovala za Yohane M’batizi Komanso Maonekedwe Ake” “Dzombe” “Uchi” zithunzi ndi mavidiyo za pa Mat. 3:4, nwtsty)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Mat. 1:3​—N’chifukwa chiyani Mateyu pofotokoza mzere womwe Yesu anabadwira anaphatikizapo mayina a azimayi 5? (“Tamara” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 1:3, nwtsty)

  • Mat. 3:11​—Kodi tikudziwa bwanji kuti munthu amene akubatizidwa ayenera kuviikidwa m’madzi? (“ndikukubatizani” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 3:11, nwtsty)

  • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mat. 1:1-17

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.

 • Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Onani chitsanzo cha ulaliki.

 • Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) bhs 41-42 ¶6-7

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 72

 • Lipoti la Chaka Chautumiki: (15 min.) Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Pambuyo powerenga kalata yochokera ku ofesi ya nthambi yonena za lipoti la chaka chautumiki chapitachi, funsani ofalitsa omwe munawasankhiratu, omwe anakumana ndi zinthu zosangalatsa m’chakacho.

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu  12 ¶9-15, bokosi patsamba 122-123, komanso tsamba 130-131

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 137 ndi Pemphero