Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Akugawira kapepala kufupi ndi mzinda wa Monrovia ku Liberia

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU January 2018

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za ulaliki zosonyeza kuti Baibulo ndi lothandizabe masiku ano.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Ufumu Wakumwamba Wayandikira”

Yohane ankakhala moyo wosalira zambiri komanso anali wodzipereka pochita chifuniro cha Mulungu. Masiku ano, kukhala moyo wosalira zambiri kungatithandize kuti tizichita zambiri potumikira Mulungu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Zimene Tikuphunzira pa Zomwe Yesu Anaphunzitsa pa Ulaliki Wapaphiri

Kodi kuzindikira zosowa zathu zauzimu kumatanthauza chiyani? Kodi tingatani kuti nthawi zonse tizikonda kuphunzira Mawu a Mulungu?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Tingatsatire Bwanji Malangizo Akuti Ukayanjane Ndi M’bale Wako Choyamba?

Kodi Yesu anasonyeza kuti pali kugwirizana kotani pakati pa kukhazikitsa mtendere ndi m’bale wathu komanso kulambira kwathu?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Pitirizani Kufunafuna Ufumu Choyamba

Kodi ndi zinthu ziti zomwe ziyenera kukhala pamalo oyamba tikamapemphera?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Musamade Nkhawa

Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anauza ophunzira ake kuti asamade nkhawa pa ulaliki wake wapaphiri?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yesu Ankakonda Anthu

Pamene Yesu anachiritsa anthu anasonyeza kuti ali ndi mphamvu. Koma chofunika kwambiri n’chakuti anasonyeza kuti amakonda anthu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yesu Ankatsitsimula Ena

Pamene tinabatizidwa, tinasenza goli la Yesu ndipo tinakhala ophunzira ake. Pa nthawiyi tinasenza udindo waukulu komanso tinayamba kugwira ntchito yolalikira yomwe si yophweka. Komabe kuchita zimenezi n’kotsitsimula.