Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za Ulaliki

NSANJA YA OLONDA

Funso: Anthu ena amaganiza kuti Baibulo ndi lachikale, pomwe ena amaona kuti ndi lothandizabe. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Lemba: 2 Tim. 3:16, 17

Perekani Magaziniyo: Nsanja ya Olonda iyi ikusonyeza kuti m’Baibulo muli malangizo anzeru komanso ikufotokoza zimene mungachite kuti muzipindula kwambiri mukamawerenga Baibulo.

KUPHUNZITSA CHOONADI

Funso: Kodi n’zoona kuti mapeto a dzikoli ali pafupi?

Lemba: Mat. 24:3, 7, 14

Zoona Zake: Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza. Mfundoyi ndi yosangalatsa chifukwa ikusonyeza kuti mavuto athu atsala pang’ono kutha.

KODI MUKUFUNA KUDZIWA CHOONADI?

Funso: Kodi Mulungu amatiganiziradi?

Lemba: 1 Pet. 5:6, 7

Perekani Kapepalako: Kapepalaka kali ndi malemba ena amene akuyankha funsoli komanso kali ndi mayankho a mafunso ena 5 ofunika kwambiri.

LEMBANI ULALIKI WANUWANU

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.