Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU–NDANDANDA YA MISONKHANO JANUARY 2017

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 29-33

“Mfumu Idzalamulira Mwachilungamo”

“Mfumu Idzalamulira Mwachilungamo”

Yesu, yemwe ndi Mfumu, amapereka “akalonga” kapena kuti akulu amene amasamalira nkhosa

32:1-3

  • Mofanana ndi “malo ousapo mvula yamkuntho,” iwo amayesetsa kuteteza nkhosa ngati zikuzunzidwa komanso amazilimbikitsa zikafooka

  • Mofanana ndi “mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi,” iwo amatsitsimula nkhosa zimene zili ndi ludzu poziphunzitsa mfundo zolondola za choonadi

  • Mofanana ndi “mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko louma,” iwo amatonthoza nkhosa pozipatsa malangizo olimbikitsa a m’Baibulo