• Nyimbo Na. 123 ndi Pemphero

 • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Mfumu Idzalamulira Mwachilungamo”: (10 min.)

  • Yes. 32:1—Mfumu imene idzalamulire mwachilungamo ndi Yesu Khristu (w14 2/15 6 ¶13)

  • Yes. 32:2—Yesu, yemwe ndi Mfumu, amapereka akalonga kuti azisamalira nkhosa (ip-1 332-334 ¶7-8)

  • Yes. 32:3, 4—Anthu a Yehova amaphunzitsidwa ndiponso kupatsidwa malangizo amene amawathandiza kuchita zinthu mwachilungamo (ip-1 334-335 ¶10-11)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Yes. 30:21—Kodi Yehova amalankhula bwanji ndi atumiki ake? (w14 8/15 21 ¶2)

  • Yes. 33:22—Kodi Yehova anakhala bwanji Woweruza, Wopereka Malamulo komanso Mfumu ya Aisiraeli, nanga anakhala liti? (w14 10/15 14 ¶4)

  • Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yes. 30:22-33

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) wp17.1 chikutoSonyezani mmene tingayankhire munthu yemwe wakwiya kwambiri.

 • Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) wp17.1 chikutoWerengani malemba pogwiritsa ntchito foni kapena tabuleti.

 • Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) lv 31-32 ¶12-13—Sonyezani mmene tingafikire pamtima wophunzira wathu.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 119

 • “Malo Obisalirapo Mphepo” (Yes. 32:2): (9 min.) Onetsani vidiyo.

 • “Muzimvetsera Tikakhala Pamisonkhano”: (6 min.) Onetsani vidiyo yakuti Muzimvetsera Tikakhala Pamisonkhano.” Kenako pemphani ana amene munawasankhiratu kuti abwere kupulatifomu ndipo muwafunse kuti: Kodi n’chiyani chimene chingakulepheretseni kumvetsera pamisonkhano? N’chiyani chimene chikanachitika Nowa akanapanda kumvetsera zimene Yehova anamuuza zokhudza mmene angakhomere chingalawa? N’chifukwa chiyani ana ayenera kumvetsera pamisonkhano?

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 15 ¶1-14 komanso bokosi patsamba 138

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 40 ndi Pemphero