Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU–NDANDANDA YA MISONKHANO JANUARY 2017

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 24-28

Yehova Amasamalira Anthu Ake

Yehova Amasamalira Anthu Ake

Yehova ndi wowolowa manja ndipo amatipatsa chakudya chambiri chauzimu.

‘Yehova wa makamu adzakonzera anthu a mitundu yonse phwando’

25:6

  • Kale, kudyera limodzi chakudya kunkasonyeza kuti anthuwo ndi ogwirizana komanso okondana

“La zakudya zabwinozabwino zokhala ndi mafuta a m’mafupa, ndiponso la vinyo wokoma kwambiri, wosefedwa bwino”

  • Zakudya zabwinozabwino ndiponso vinyo wokoma kwambiri komanso wosefedwa bwino zikuimira chakudya chauzimu chabwino kwambiri chimene Yehova amatipatsa