Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  January 2017

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 38-42

Yehova Amapereka Mphamvu kwa Munthu Wotopa

Yehova Amapereka Mphamvu kwa Munthu Wotopa

40:29-31

  • Chiwombankhanga chikhoza kuuluka nthawi yaitali pogwiritsa ntchito mpweya wotentha. Chikafika pamene pakuwomba mpweyawu chimauluka mozungulira pamwamba pa mpweyawo ndipo chimakankhidwa mpaka kupita m’mwamba. Chikafika m’mwambamo, chimafufuza pomwe pali mpweya wina wotentha womwe umachikankhanso mpaka m’mwamba kwambiri

  • Zimene zimachitika kuti chiwombankhanga chizitha kuuluka kwa nthawi yaitali zikufanana ndi mmene Yehova amatipatsira mphamvu kuti tisatope pomutumikira