Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  January 2017

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Inu Yehova, . . . Chikhulupiriro Changa Chili mwa Inu”

“Inu Yehova, . . . Chikhulupiriro Changa Chili mwa Inu”

Tiyenera kukhulupirira Yehova tikakhala pa mtendere ngakhalenso pa mavuto. (Sal. 25:1, 2) M’zaka za m’ma 700 B.C.E., Ayuda amene anali ku Yuda anakumana ndi mavuto omwe anayesa chikhulupiriro chawo. Tingaphunzire zambiri pa zomwe zinawachitikirazi. (Aroma 15:4) Kambiranani mafunso otsatirawa okhudza vidiyo yakuti “Inu Yehova, . . . Chikhulupiriro Changa Chili mwa Inu.”

  1. Kodi Hezekiya anakumana ndi mavuto otani?

  2. Kodi Hezekiya anagwiritsa ntchito bwanji mfundo ya pa Miyambo 22:3 pokonzekera kubwera kwa Asuri?

  3. N’chifukwa chiyani Hezekiya sanadzipereke kwa Asuri kapena kupanga mgwirizano ndi Aiguputo?

  4. N’chifukwa chiyani Hezekiya ndi chitsanzo chabwino kwa Akhristu?

  5. Kodi ndi zinthu ziti masiku ano zimene zingayese chikhulupiriro chathu?

Lembani mbali zimene mukuona kuti mukuyenera kumadalira kwambiri Yehova . . .