Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  January 2017

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 34-37

Hezekiya Anadalitsidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake

Hezekiya Anadalitsidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake

Senakeribu, yemwe anali mfumu ya Asuri, anatumiza Rabisake ku Yerusalemu kuti akakakamize Ayuda amumzindawo kuti angodzipereka okha. Asuriwo ananena mfundo zambiri zoopseza n’cholinga choti Ayuda achite mantha n’kudzipereka okha kwa Asuri popanda kumenya nkhondo

  • Anawauza kuti adzasowa owathandiza. Aiguputo sangakuthandizeni.—Yes. 36:6

  • Anawapangitsa kukayikira za Yehova. Yehova sakumenyerani nkhondo chifukwa sakusangalala nanu.—Yes. 36:7, 10

  • Anawaopseza. Musaganize n’komwe zoti mungalimbane ndi asilikali amphamvu a Asuri.—Yes. 36:8, 9

  • Anawanyengerera. Mukadzipereka nokha kwa Asuri zinthu zikuyenderani bwino pa moyo wanu.—Yes. 36:16, 17

Hezekiya sanasiye kukhulupirira Yehova

37:1, 2, 14-20, 36

  • Anayesetsa kuchita zinthu mwanzeru pokonzekera kubwera kwa Asuri

  • Anapemphera kwa Yehova kuti awapulumutse komanso analimbikitsa anthu onse kuti azipemphera

  • Yehova anadalitsa Hezekiya chifukwa cha chikhulupiriro chake moti anatumiza mngelo kuti akaphe asilikali a Asuri okwana 185,000 usiku umodzi wokha