Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ntchito yolalikira uthenga wabwino ku Ghana

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU January 2017

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za ulaliki wa Nsanja ya Olonda ndiponso zomwe tingachite pophunzitsa anthu chizindikiro cha masiku otsiriza. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mupange ulaliki wanuwanu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yehova Amasamalira Anthu Ake

Yehova ndi wowolowa manja ndipo amatipatsa chakudya chambiri chauzimu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Mfumu Idzalamulira Mwachilungamo”

Yesu, yemwe ndi Mfumu, amakonza zoti pakhale akulu omwe amasamalira nkhosa. Amatsitsimula nkhosazo pozitsogolera pa zinthu zauzimu komanso kuzilimbikitsa.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Hezekiya Anadalitsidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake

Asuri ankafuna kuti Ayuda achite mantha n’kudzipereka okha popanda kumenya nkhondo, koma yehova anatumiza mngelo wake kuti akateteze mzinda wa Yerusalemu.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Inu Yehova, . . . Chikhulupiriro Changa Chili mwa Inu”

Tiyenera kukhulupirira Yehova tikakhala pa mtendere komanso pa mavuto. Kodi Hezekiya anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira Mulungu?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yehova Amapereka Mphamvu kwa Munthu Wotopa

Zimene zimachitika ndi chiwombankhanga zikufanana ndi mmene Yehova amatipatsira mphamvu kuti tisatope pomutumikira.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tisamaiwale Kupempherera Akhristu Amene Akuzunzidwa

Kodi tinganene chiyani popempherera Akhristu amene akuzunzidwa?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yehova Ndi Mulungu Yemwe Amalosera Zoona

Yehova Mulungu anagwiritsa ntchito Yesaya kuti alosere zimene zidzachitikire Babulo patapita zaka 200.