NSANJA YA OLONDA

Funso: Kodi aliyense akanakhala kuti amatsatira mfundo iyi, bwenzi zinthu zili bwanji m’dzikoli?

Lemba: Aheb. 13:18

Perekani Magaziniyo: Baibulo limatilimbikitsa kuti tizikhala oona mtima pa zonse zimene timachita. Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza nkhani imeneyi.

NSANJA YA OLONDA (tsamba lomaliza)

Funso: Ndikufuna ndimve maganizo anu pa funso ili. [Werengani Funso loyamba.] Anthu ena amakhulupirira kuti akamwalira, chinachake chimakhalabe ndi moyo, koma ena amati imfa ndi mapeto a zonse. Kodi inuyo mumakhulupirira chiyani?

Lemba: Mlal. 9:5

Perekani Magaziniyo: Mutu uwu ukufotokoza zimene Baibulo limanena pankhaniyi. Ndikusiyirani kuti muwerenge kenako tidzakambirane paulendo wotsatira.

UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU!

Perekani Kabukuko: Ndimati ndikupempheni kuti ndiziphunzira nanu Baibulo kwaulere. Kabuku aka kangakuthandizeni kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri m’Baibulo.

Funso: Kodi inuyo munawerengapo Baibulo? Kuphunzira kwake n’kosavuta. Bwanji ndikusonyezeni? [Kambiranani funso loyamba la Phunziro 2.]

Lemba: Chiv. 4:11

LEMBANI NJIRA INA IMENE MUNGAGWIRITSE NTCHITO

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.