N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUCHITA ZIMENEZI?

Tikalalikira munthu, zimakhala ngati tabzala mbewu ndipo mbewuzo zimafunika kuzithirira. (1 Akor. 3:6) Choncho tikakumana ndi munthu amene akufunitsitsa kuphunzira, tiyenera kusiya funso loti tidzakambirane ulendo wotsatira. Tikatero, munthuyo amatiyembekezera mwachidwi ndipo sitivutika pokonzekera ulendo wobwereza. Ndiyeno tikafika tingamuuze kuti tabwera kudzayankha funso lija.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Mukamakonzekera kulalikira nyumba ndi nyumba muzipezeratu funso limene mungasiye kuti mudzayankhe pa ulendo wobwereza. Funsolo lizikhala loti yankho lake lili m’magazini amene mukugawira kapena m’buku lina limene timagwiritsa ntchito pophunzira ndi anthu.

  • Posiyana ndi munthu amene ali ndi chidwi, muzimuuza kuti mudzabweranso ndipo mufunseni funso limene munaliganizira kale kuti mudzakambirane pa ulendo wotsatira. Muzilemba zinthu monga dzina lake, kumene akukhala komanso nambala ya foni ngati angalole.

  • Mukalonjeza kuti mudzapita tsiku lina, pa nthawi inayake, musalephere kupitako.—Mat. 5:37.