Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  January 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZARA 6-10

Yehova Amafuna Kuti Tizimutumikira ndi Mtima Wonse

Yehova Amafuna Kuti Tizimutumikira ndi Mtima Wonse

Ezara anakonzekera kubwerera ku Yerusalemu

7:6, 22; 8:26, 27

  • Ezara analoledwa ndi Mfumu Aritasasita kuti apite ku Yerusalemu kukathandiza anthu kuti azilambira Yehova

  • Mfumu inapatsa Ezara “zopempha zake zonse” kuti akamangire nyumba ya Yehova. Inamupatsa golide, siliva, tirigu, vinyo, mafuta ndi mchere. Malinga ndi ndalama za masiku ano, zonse zingakwane madola 100 miliyoni a ku America

Ezara ankakhulupirira kuti Yehova ateteza atumiki ake

7:13; 8:21-23

  • Ulendo wobwerera ku Yerusalemu unali wovuta

  • Unali mtunda wa makilomita pafupifupi 1,600 ndipo ankadutsa m’malo oopsa

  • Ulendowu unatenga miyezi pafupifupi 4

  • Anthu obwererawo anafunika kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu, kulimba mtima komanso kukonda kwambiri kulambira Yehova

EZARA ANATENGA . . .

Golide ndi siliva zolemera matalente oposa 750

MAVUTO AMENE ANTHU ANAKUMANA NAWO POBWERERA . . .

Magulu a zigawenga, kutentha kwa m’chipululu, zilombo zolusa