Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

January 18-24

EZARA 1-5

January 18-24
 • Nyimbo Na. 85 ndi Pemphero

 • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Yehova Amakwaniritsa Malonjezo Ake”: (10 min.) [Onetsani vidiyo ya Ezara.]

  • Ezara 3:1-6—Zimene Yehova walonjeza sizilephereka (w06 1/15 19 ndime 2)

  • Ezara 5:1-7—Yehova akhoza kusintha zinthu kuti anthu ake ziwayendere (w06 1/15 19 ndime 4; w86-E 1/15 9 ndime 2; w86-E 2/1 29 bokosi)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Ezara 1:3-6—Kodi Aisiraeli amene sanapite nawo ku Yerusalemu anali ndi chikhulupiriro chochepa? (w06 1/15 17 ndime 5 komanso tsa. 19 ndime 1)

  • Ezara 4:1-3—N’chifukwa chiyani anakana kuthandizidwa? (w06 1/15 19 ndime 3)

  • Kodi ndaphunzira chiyani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?

 • Kuwerenga Baibulo: Ezara 3:10–4:7 (Osapitirira 4 min.)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gawirani magazini a January pogwiritsa ntchito nkhani yomaliza m’magazini a Nsanja ya Olonda ya mwezi uno. Muuzeni zimene mudzakambirane ulendo wotsatira.

 • Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Chitani chitsanzo chosonyeza munthu akuchita ulendo wobwereza kwa munthu amene tinamupatsa Nsanja ya Olonda pogwiritsa ntchito tsamba lomaliza. Muuzeni nkhani imene mudzaphunzire ulendo wotsatira.

 • Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) Chitani chitsanzo cha munthu akuchititsa phunziro la Baibulo. (bh tsa. 20-21 ndime 6-8)

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 40

 • “Zina Zonsezi Zidzawonjezedwa kwa Inu”: (5 min.) Nkhani yochokera pa Mateyu 6:33 ndi Luka 12:22-24. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene zinawachitikira zosonyeza kuti Yehova anakwaniritsa lonjezo loti adzawapatsa zina zonse ngati ataika Ufumu pamalo oyamba.

 • Mawu Anu Asakhale, Inde Kenako Ayi: (10 min.) Nkhani yokambirana (w14 3/15 30-32)

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: cl mutu 24 ndime 18-21 ndi bokosi patsamba 249 (30 min.)

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu wa Mawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 41 ndi Pemphero