Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  January 2016

January 11-17

2 MBIRI 33-36

January 11-17
 • Nyimbo Na. 35 ndi Pemphero

 • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Yehova Amakhululukira Munthu Amene Walapa Kuchokera Pansi pa Mtima”: (10 min.)

  • 2 Mbiri 33:2-9, 12-16—Mulungu anakhululukira Manase chifukwa analapa kuchokera pansi pa mtima (w05 12/1 21 ndime 6)

  • 2 Mbiri 34:18, 30, 33—Kuwerenga Baibulo komanso kuganizira mfundo zake kungatithandize (w05 12/1 21 ndime 11)

  • 2 Mbiri 36:15-17—Sitiyenera kuchita dala zinthu zoipa poganiza kuti Yehova atikhululukira (w05 12/1 21 ndime 8)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • 2 Mbiri 33:11—Kodi ndi ulosi uti umene unakwaniritsidwa Manase atatengedwa kupita ku Babulo? (w06 12/1 9 ndime 5)

  • 2 Mbiri 34:1-3—Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yosiya? (w05 12/1 21 ndime 7)

  • Kodi ndaphunzira chiyani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?

 • Kuwerenga Baibulo: 2 Mbiri 34:22-33 (Osapitirira 4 min.)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gawirani magazini a mwezi wa uno pogwiritsa ntchito mutu wa Nsanja ya Olonda. Muuzeni zimene mudzakambirane mukadzabweranso.

 • Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Chitani chitsanzo chosonyeza kuti mwakumananso ndi munthu amene munampatsa magazini a mwezi uno pogwiritsira ntchito mutu wa magaziniyi. Muuzeni nkhani yomwe mudzaphunzire mukadzabweranso.

 • Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) Chitani chitsanzo chosonyeza mukuphunzira ndi munthu. (bh tsa. 9-10 ndime 6 ndi 7)

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 77

 • Munthu Akalapa Zinthu Zimamuyendera Bwino. (10 min.) Nkhani yokambidwa ndi mkulu. (w06 11/15 27-28 ndime 7-9)

 • Uzikhululuka ndi Mtima Wonse. (5 min.) Nkhani yokambirana. Onetsani vidiyo yakuti Uzikhululuka ndi Mtima Wonse. (Vidiyoyi ikupezeka pa webusaiti yathu ya jw.org/ny, pamene alemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANA.) Kenako pemphani ana kuti afotokoze zimene akuphunzirapo.

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: cl mutu 24 ndime 11-17 (30 min.)

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu wa Mawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 6 ndi Pemphero