1. Werengani funso limene lalembedwa m’zilembo zakuda kwambiri kuti mwininyumba aganizire kwambiri mfundo yaikulu.

  2. Werengani ndime yake.

  3. Werengani malemba akuda kwambiri ndipo funsani mafunso amene angathandize munthuyo kuti apeze yankho la funso lija pa ndimeyo.

  4. Ngati m’munsi mwa funsolo muli ndime inanso, bwerezani mfundo 2 ndi 3. Ngati pa jw.org/ny pali vidiyo yomwe ikugwirizana mafunsowo, muonetseni mwininyumbayo.

  5. Kuti mutsimikizire ngati mwininyumbayo wamvetsa mfundo yaikulu, mufunseni mafunso akuda kwambiri aja.