Ntchito yomanga kachisi wa Yehova inali yaikulu. Koma Aisiraeli anadzipereka kwambiri mpaka anamaliza. (1 Mbiri 29:2-9; 2 Mbiri 6:7, 8) Kachisiyu atamalizidwa, ankafunika kukonzedwanso. Ndiyeno zimene Aisiraeli ankachita pa ntchito yokonzayi zinkasonyeza ngati amakonda Yehova kapena ayi. (2 Maf. 22:3-6; 2 Mbiri 28:24; 29:3) Masiku anonso, Akhristu amadzipereka kwambiri pa ntchito yomanga, kukonza komanso kuyeretsa Nyumba za Ufumu ndi Malo a Misonkhano. Ndi mwayi waukulu kugwira nawo ntchito zimenezi chifukwa ndi utumiki wopatulika.—Sal. 127:1; Chiv. 7:15.

ZIMENE TINGACHITE

  • Kuyeretsa malo tikangomaliza misonkhano. Ngati tilibiretu nthawi tikhoza kungotola tizinyalala pafupi ndi pamene takhala.

  • Tizigwira nawo ntchito yoyeretsa kapena kukonza Nyumba ya Ufumu. Ntchito ikamagwiridwa ndi anthu ambiri imasangalatsa komanso imapepuka.—lv 92-93 ndime 18.

  • Tizipereka ndalama zothandiza pa ntchitoyi. Yehova amasangalala kwambiri ngakhale ndalama zathuzo zitakhala ngati ‘timakobidi tiwiri tating’ono.’—Maliko 12:41-44.

  • Ngati n’zotheka tizidzipereka kugwira nawo ntchito yomanga komanso kukonza malo olambirira. Sikuti tiyenera kukhala ndi luso lapadera kuti tigwire nawo ntchitoyi.