KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Anthu ayenera kuitanira pa dzina la Yehova kuti adzapulumuke. (Aroma 10:13, 14) Komabe si anthu onse amene timaphunzira nawo Baibulo omwe amafuna kutsatira mfundo za Yehova. Choncho timafunika kugwiritsa ntchito bwino nthawi yathu tikakhala mu utumiki n’cholinga choti tithandize anthu amene amafuna kusintha moyo wawo kuti asangalatse Yehova. Ngati munthu sakupita patsogolo titaphunzira naye kwa nthawi yaitali ndithu, tiyenera kumusiya n’kupitiriza kufufuza anthu amene Yehova angawakoke n’kuwabweretsa m’gulu lake. (Yoh. 6:44) Koma ngati n’kupita kwa nthawi wayamba kusonyeza kuti ali ‘ndi maganizo abwino amene angamuthandize kudzapeza moyo wosatha,’ tikhoza kuyambiranso kuphunzira naye.​—Mac. 13:48.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Muyamikireni chifukwa cha mtima wake wofuna kudziwa zolondola zokhudza Baibulo.​—1 Tim. 2:4

  • Muuzeni kufunika kogwiritsa ntchito zimene waphunzira.—Luka 6:46-49

  • Kambiranani naye mwachikondi fanizo la Yesu la wofesa mbewu, ndipo muuzeni kuti aganizire zinthu zomwe zikumuchititsa kuti asapite patsogolo.—Mat. 13:18-23

  • Mosamala kwambiri mufotokozereni chifukwa chimene mukusiyira kuphunzira naye

  • Muuzeni kuti muzimuyendera nthawi zina kuti mumulimbikitse. Muuzeninso kuti mukhoza kudzayambiranso kuphunzira m’tsogolo ngati atayamba kusintha

ONERANI VIDIYO NDIPO KENAKO KAMBIRANANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Malinga ndi vidiyoyi, n’chiyani chimene chikusonyeza kuti wophunzirayu sakupita patsogolo?

  • Kodi wofalitsayu anathandiza bwanji wophunzira wakeyu kuzindikira kuti akufunika kusintha?

  • Kodi wofalitsayu wathandiza bwanji wophunzirayo kudziwa kuti ngati atasintha akhoza kudzayambiranso kuphunzira m’tsogolo?