5:8, 18, 21

Nsembe ya dipo ya Yesu imathandiza kumvetsa nkhani zofunika kwambiri monga ya kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu komanso kudziwa kuti Yehova yekha ndiye woyenera kulamulira. Nsembeyi imathandizanso kuti Yehova azitiona kuti ndife olungama ndiponso kuti tidzapeze moyo wosatha umene adzapereke kwa anthu omvera.

Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira nsembe ya dipo?

  • Kudzipereka komanso kubatizidwa kumasonyeza kuti ndife okhulupirika ndipo tikufuna kukhala anthu a Yehova

  • Tikamalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu timasonyeza kuti timatsanzira Yehova pankhani yokonda anthu amitundu yonse.​—Mat. 22:39; Yoh. 3:16

Kodi ndingasonyeze m’njira zinanso ziti kuti ndimayamikira nsembe ya dipo imene Yehova anapereka?