CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Mulungu Akuonetsa Chikondi Chake Kwa Ife”: (10 min.)

  • Aroma 5:8, 12​—Yehova anatikonda ngakhale kuti ndife “ochimwa” (w11 6/15 12 ¶5)

  • Aroma 5:13, 14​—Uchimo ndi imfa zakhala zikulamulira ngati mfumu (w11 6/15 12 ¶6)

  • Aroma 5:18, 21​—Yehova anatumiza Mwana wake kuti tidzapeze moyo (w11 6/15 12-13 ¶9-10)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Aroma 6:3-5​—Kodi kubatizidwa “mu mgwirizano ndi Khristu Yesu” komanso “mu imfa yake” kumatanthauza chiyani? (w08 6/15 29 ¶7)

  • Aroma 6:7​—N’chifukwa chiyani anthu amene adzaukitsidwe sadzaweruzidwa chifukwa cha machimo amene anachita asanamwalire? (w14 6/1 11 ¶1)

  • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Aroma 4:1-15 (th phunziro 10)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

MOYO WATHU WACHIKHRISTU