●○○ ULENDO WOYAMBA

Funso: Kodi inuyo mumaona kuti Baibulo ndi lothandizabe masiku ano?

Lemba: 2 Tim. 3:16

Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi zimene Baibulo limanena zimagwirizana ndi sayansi?

○●○ ULENDO WOBWEREZA WOYAMBA

Funso: Kodi zimene Baibulo limanena zimagwirizana ndi sayansi?

Lemba: Yobu 26:7

Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi malangizo a m’Baibulo ndi othandizadi?

○●○ ULENDO WOBWEREZA WACHIWIRI

Funso: Kodi malangizo a m’Baibulo ndi othandizadi?

Lemba: Miy. 14:30

Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi Baibulo limalosera zolondola ponena zam’tsogolo?