KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Ngati “maganizo a mumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya,” ndiye kuti mafunso ali ngati chotungira madziwo. (Miy. 20:5) Mafunso amathandiza kuti omvera afotokoze maganizo awo ndipo zingatithandize kudziwa mmene tingawathandizire. Yesu ankagwiritsa ntchito mafunso mwaluso. Ndiye kodi ifeyo tingamutsanzire bwanji?

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Muzifunsa mafunso omwe angachititse munthu kufotokoza maganizo ake. Yesu ankakonda kufunsa mafunso amene ankachititsa ophunzira ake kufotokoza maganizo awo. (Mat. 16:13-16; be 238 ¶3-5) Kodi mungafunse mafunso ati kuti mudziwe maganizo a wophunzira wanu?

  • Muzifunsa mafunso othandiza munthu kupeza yekha yankho lolondola. Pofuna kuthandiza Petulo kukhala ndi maganizo oyenera, Yesu anamufunsa mafunso omuthandiza kupeza yankho lolondola. (Mat. 17:24-26) Kodi mungafunse mafunso ati pofuna kuthandiza wophunzira kuti apeze yekha yankho lolondola?

  • Muzimuyamikira wophunzira wanu. Mlembi wina ‘atayankha mwanzeru,’ Yesu anamuyamikira. (Maliko 12:34) Kodi mungayamikire bwanji wophunzira ngati wayankha funso limene mwafunsa?

ONERANI MBALI YOYAMBA YA VIDIYO YAKUTI MUZIGWIRA NTCHITO IMENE YESU ANAGWIRA​—MUZIPHUNZITSA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • N’chifukwa chiyani kumeneku sikuphunzitsa kwabwino ngakhale kuti mfundozo n’zolondola?

  • N’chifukwa chiyani kuphunzitsa kumafuna zambiri osati kungofotokoza mfundo?

ONERANI MBALI YACHIWIRI YA VIDIYOYI KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi m’baleyu wagwiritsa ntchito bwanji mafunso mwaluso?

  • Kodi ndi zinthu zina ziti zimene m’baleyu wachita zomwe tingatengere?

Kodi zimene timaphunzitsa zimakhudza bwanji anthu ena? (Luka 24:32)