Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  February 2017

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za Ulaliki

GALAMUKANI!

Funso: Zikuoneka kuti achinyamata ambiri masiku ano akudwala matenda ovutika maganizo. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chingathandize kuchepetsa vutoli?

Perekani Magaziniyo: Magazini iyi ikufotokoza mfundo zimene zingathandize achinyamata amene akudwala matendawa ndiponso mmene makolo awo angawathandizire.

KUPHUNZITSA CHOONADI

Funso: Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhale ndi banja losangalala?

Lemba: Aef. 5:33

Zoona Zake: Banja limayenda bwino mwamuna ndi mkazi akamakondana ndiponso kulemekezana.

KODI BAIBULO LILI NDI UTHENGA WOTANI? (bm)

Funso: Anthu ambiri amene talankhula nawo amadandaula chifukwa cha zinthu zoipa zimene zikuchitika m’dzikoli. Kodi mukuganiza kuti Mulungu adzathetsa mavutowa?

Lemba: Sal. 37:11

Perekani Kabukuko: Baibulo limanena kuti posachedwapa Mulungu athetsa mavuto. Limafotokozanso mfundo zimene zingatithandize kulimbana ndi mavuto athu panopa. Kabuku aka kakufotokoza zambiri pa nkhaniyi.

LEMBANI ULALIKI WANUWANU

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.