Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU–NDANDANDA YA MISONKHANO FEBRUARY 2017

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 47-51

Kumvera Yehova Kumabweretsa Madalitso

Kumvera Yehova Kumabweretsa Madalitso

48:17

  • Yehova amatisonyeza mwachikondi ‘njira imene tiyenera kuyendamo’ n’cholinga choti tizikhala osangalala. Tikamamumvera zinthu zimatiyendera bwino.

“Mtendere . . . ngati mtsinje”

48:18

  • Yehova akulonjeza kuti tingakhale ndi mtendere wochuluka ndiponso wosatha ngati mtsinje womwe susiya kuyenda

“Chilungamo . . . ngati mafunde a m’nyanja”

  • Tidzatha kuchita zinthu zachilungamo zosawerengeka ngati mafunde a m’nyanja