Chilengedwe chimalengeza ulemerero wa Yehova. (Sal. 19:1-4; 139:14) Komabe dziko la Mdyerekezili limalimbikitsa mfundo zonyoza Mulungu pa nkhani ya mmene moyo unayambira. (Aroma 1:18-25) Kodi mungatani kuti mfundo zimenezi zisazike mizu m’maganizo ndiponso mumtima mwa ana anu? Muyenera kuwathandiza kuyambira ali aang’ono kuti azikhulupirira Yehova ndiponso kudziwa kuti iye amawakonda. (2 Akor. 10:4, 5; Aef. 6:16) Muzikambirana nawo kuti mudziwe maganizo awo pa nkhani zimene amaphunzira kusukulu. Kuti muziwafika pamtima, muzigwiritsa ntchito mabuku, webusaiti yathu ndiponso mavidiyo.Miy. 20:5; Yak. 1:19.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA—KUKHULUPIRIRA KUTI KULI MULUNGU, NDIPO KENAKO KAMBIRANANI NAWO MAFUNSO AWA:

  • Kodi anthu ambiri amanena zotani pa nkhani ya kukhulupirira Mulungu?

  • Kodi kusukulu kwanu amaphunzitsa zotani pa nkhaniyi?

  • N’chiyani chimakutsimikizirani kuti Yehova alipodi?

  • Kodi mungathandize bwanji munthu kuzindikira kuti Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse?