Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  February 2017

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizisangalala ndi Chiyembekezo Chathu

Tizisangalala ndi Chiyembekezo Chathu

Chiyembekezo chili ngati nangula amene amathandiza kuti sitima isasunthe. (Aheb. 6:19) Zili choncho chifukwa chimatithandiza kuti tisasokonezeke mwauzimu tikakumana ndi mavuto aakulu okhala ngati mafunde oopsa. (1 Tim. 1:18, 19) Mavutowa akhoza kukhala matenda aakulu, mavuto azachuma, imfa ya munthu amene tinkamukonda kapena mayesero ena alionse.

Chikhulupiriro komanso chiyembekezo chimatithandiza kuti tisamakayikire ngakhale pang’ono zimene Mulungu watilonjeza. (2 Akor. 4:16-18; Aheb. 11:13, 26, 27) Choncho kaya tikuyembekezera kupita kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi, tiyenera kumaganizira kwambiri zimene Mulungu walonjeza m’Mawu ake. Kuchita zimenezi kungatithandize kukhalabe osangalala pamene takumana ndi mayesero.1 Pet. 1:6, 7.

ONERANI VIDIYO YAKUTI TIZISANGALALA NDI CHIYEMBEKEZO CHATHU. KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • N’chifukwa chiyani Mose ndi chitsanzo chabwino?

  • Kodi amuna okwatira ali ndi udindo wotani m’banja?

  • Kodi ndi nkhani ziti zimene mungakambirane pa Kulambira kwa Pabanja?

  • Kodi kukhala ndi chiyembekezo kungakuthandizeni bwanji kuti musataye mtima mukakumana ndi mayesero?

  • Kodi inuyo mukuyembekezera zinthu ziti?