Zimene Mulungu analonjeza mu chaputala 65 cha Yesaya zidzachitikadi ndipo n’chifukwa chake Yehova anazinena ngati zachitika kale

Yehova akulenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano ndipo zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso

65:17

Kodi kumwamba kwatsopano n’chiyani?

  • Boma latsopano limene lidzathetse zinthu zopanda chilungamo padzikoli

  • Linakhazikitsidwa mu 1914 pamene Khristu anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu

Kodi dziko lapansi latsopano n’chiyani?

  • Anthu ochokera m’mayiko, zinenero komanso m’mitundu yosiyanasiyana omwe amamvera ndi mtima wonse boma latsopano la kumwamba

Kodi mawu akuti zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso akutanthauza chiyani?

  • Mulungu adzachotsa mavuto onse amene amachititsa kuti tizikumbukira zinthu zoipa zimene zinatichitikira.

  • Anthu okhulupirika adzasangalala kwambiri ndi moyo ndipo tsiku lililonse azidzachita zinthu zoti akazikumbukira, zizidzawasangalatsa