Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  February 2017

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 58-62

‘Tikalengeze za Chaka cha Yehova Chokomera Anthu Mtima’

‘Tikalengeze za Chaka cha Yehova Chokomera Anthu Mtima’

Sikuti “chaka cha Yehova chokomera anthu mtima” ndi chaka chenicheni

61:1, 2

  • Ndi nthawi imene Yehova amapatsa anthu ofatsa mwayi woti alandire ufulu

  • Kale, chaka chokomera anthu mtima chinayamba pamene Yesu anayamba utumiki wake mu 29 C.E. ndipo chinatha pa “tsiku lobwezera” la Yehova pamene Yerusalemu anawonongedwa mu 70 C.E.

  • M’nthawi yathu ino, chaka chokomera anthu mtima chinayamba pamene Yesu anakhala mfumu kumwamba mu 1914 ndipo chidzatha pa chisautso chachikulu

Yehova amadalitsa anthu ake powapatsa “mitengo ikuluikulu ya chilungamo”

61:3, 4

  • Nthawi zambiri, mitengo ikuluikulu kwambiri imapezeka m’nkhalango

  • Mizu ya mitengoyi imalukana ndipo zimenezi zimathandiza kuti mitengoyi isagwe kukakhala mphepo yamphamvu

  • Mitengo ikuluikuluyi imateteza timitengo ting’onoting’ono ku dzuwa ndipo masamba ake akayoyoka amawonjezera chonde m’nthaka

Anthu onse amumpingo wachikhristu wa padziko lonse amathandizidwa ndiponso kutetezedwa ndi “mitengo ikuluikulu ya chilungamo,” yomwe ikuimira Akhristu odzozedwa amene adakali padzikoli