Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU–NDANDANDA YA MISONKHANO FEBRUARY 2016

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za Ulaliki

GALAMUKANI!

Funso: Ndabwera kudzakupatsani magazini yatsopano ya Galamukani! Ndikufuna ndimve maganizo anu pa funso ili lomwe lili patsamba 2.

Lemba: Miy. 24:10

Perekani Magaziniyo: Nkhani imeneyi ikufotokoza mfundo zinanso zothandiza.

GALAMUKANI!

Funso: Anthu ambiri amaona kuti n’zothandiza kusankha bwino anzawo apamtima. Kodi inunso mumaona choncho?

Lemba: Miy. 13:20

Perekani Magaziniyo: Magazini iyi ili ndi mfundo zimene zingatithandize kupeza anzathu abwino apamtima. [Musonyezeni nkhani imene ili patsamba 10 ndi 11.]

MVERANI MULUNGU

Funso: Kodi mungakonde kudzakhala m’dziko looneka chonchi? [Musonyezeni tsamba 2 ndi 3, kenako yembekezani kuti ayankhe.]

Lemba: Yer. 29:11

Perekani Kabukuko: Kabuku aka kakufotokoza zimene tingachite kuti tizimvera Mulungu n’kudzalandira madalitso amene watikonzera. [Kambiranani zimene zili patsamba 4 ndi 5.]

LEMBANI NJIRA INA IMENE MUNGAGWIRITSE NTCHITO

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.