• Nyimbo Na. 106 ndi Pemphero

  • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

  • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Perekani kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso kwa munthu amene wasonyeza chidwi chochepa.

  • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 4 min.) Perekani kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso komanso Nsanja ya Olonda kwa munthu amene wasonyeza chidwi kwambiri. Muuzeni zimene mudzaphunzire ulendo wotsatira.

  • Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) Fotokozerani wophunzira mfundo zokhudza Chikumbutso pogwiritsa ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, tsamba 206-208. Muthandizeni kuti adzapezeke pamwambowu.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

  • Nyimbo Na. 5

  • Itanirani Anthu Onse M’gawo Lanu ku Chikumbutso”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Fotokozani dongosolo limene mpingo udzayendere poitanira anthu ku Chikumbutso. Pokambirana mbali yakuti “Zimene Mungachite,” onetsani vidiyo ya Chikumbutso. Limbikitsani onse kuti adzagwire nawo ntchito yoitanira anthu ku Chikumbutso ndipo adzathandize anthu amene asonyeza chidwi. Chitaninso chitsanzo.

  • Phunziro la Baibulo la Mpingo: cl mutu 26 ndime 10-17 (30 min.)

  • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu wa Mawa (3 min.)

  • Nyimbo Na. 147 ndi Pemphero