GALAMUKANI!

Funso: Anthu ambiri amafuna kukhala ndi moyo wathanzi. Kodi mukuganiza kuti tingatani kuti tidziteteze ku matenda?

Lemba: Miy. 22:3

Perekani Magaziniyo: Galamukani! iyi ikufotokoza njira zimene tingatsate kuti tidziteteze ku matenda.

KUPHUNZITSA CHOONADI

Funso: Kodi Mulungu ndi amene amayambitsa mavuto amene timakumana nawo?

Lemba: Yobu 34:10

Zoona Zake: Mulungu si amene amachititsa mavuto athu. Amene amachititsa mavuto ndi Mdyerekezi komanso anthu amene amasankha zinthu molakwika. Ndipo nthawi zina timakumana ndi mavuto chifukwa choti tinali malo olakwika pa nthawinso yolakwika. Tikakumana ndi mavuto, Mulungu amakhala wokonzeka kutithandiza chifukwa amatidera nkhawa.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUPHUNZIRA BAIBULO? (Vidiyo)

Funso: Kodi mukuganiza kuti Mulungu ndi amene akulamulira dzikoli? [Yembekezerani kuti ayankhe.] Zimene Baibulo limanena zikhoza kukudabwitsani. Tiyeni tione zimenezi m’vidiyoyi. [Onetsani vidiyoyo.]

Perekani Buku: Mutu 11 wa buku ili ukufotokoza chifukwa chake Mulungu walola kuti anthu azivutika. Ukufotokozanso kuti Mulungu athetsa mavutowa posachedwapa. [Perekani buku lakuti, Zimene Baibulo Limaphunzitsa.]

LEMBANI ULALIKI WANUWANU

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.