Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu–Ndandanda ya Misonkhano  |  December 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 17-23

Munthu Akamagwiritsa Ntchito Udindo Wake Molakwika Amachotsedwa pa Udindowo

Munthu Akamagwiritsa Ntchito Udindo Wake Molakwika Amachotsedwa pa Udindowo

Sebina anali “kapitawo woyang’anira nyumba ya mfumu,” ndipo n’kutheka kuti inali nyumba ya Mfumu Hezekiya. Pa udindo umenewu, iye anali wachiwiri kwa mfumu ndipo ankayenera kuthandiza Aisiraeli.

22:15, 16

  • Sebina ankayenera kusamalira zimene anthu a Yehova ankafunikira

  • Iye anasonyeza kudzikonda chifukwa anachita zinthu zongofuna kuti atchuke

22:20-22

  • Yehova anachotsa Sebina pa udindo wake n’kuikapo Eliyakimu

  • Eliyakimu anapatsidwa “makiyi a nyumba ya Davide,” zomwe zikuimira mphamvu komanso ulamuliro

Taganizirani izi: Kodi Sebina akanagwiritsa ntchito bwanji udindo wake kuti athandize anthu ena?