Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  December 2016

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 11-16

Dziko Lapansi Lidzadzaza ndi Anthu Odziwa Yehova

Dziko Lapansi Lidzadzaza ndi Anthu Odziwa Yehova

Mmene ulosiwu unakwaniritsidwira m’nthawi ya Aisiraeli

  • Pamene Aisiraeli ankabwerera kuchoka ku ukapolo ku Babulo ndiponso atafika kudziko lawo, sankafunika kuopa zilombo zakutchire kapena anthu amakhalidwe ngati a zilombo.—Ezara 8:21, 22.

Mmene ulosiwu ukukwaniritsidwira masiku ano

  • Kuphunzira za Yehova kwathandiza anthu ambiri kusintha makhalidwe awo. Anthu amene kale anali ankhanza asintha ndipo amakhala mwamtendere ndi anzawo. Kuphunzira za Mulungu kwathandiza kuti padziko lonse pakhale paradaiso wauzimu.

Mmene ulosiwu udzakwaniritsidwire mtsogolo

  • Dziko lonse lapansi lidzasinthidwa kuti likhale lokongola ndipo anthu azidzakhala motetezeka komanso mwamtendere ngati mmene Mulungu ankafunira poyamba. Palibe nyama iliyonse kapena munthu amene azidzapangitsa kuti anthu azikhala mwamantha.

Paulo anasintha chifukwa chophunzira za Mulungu

  • Poyamba anali Mfarisi ndipo anali ndi makhalidwe ngati a chilombo.—1 Tim. 1:13.

  • Kudziwa mfundo zolondola kunamuthandiza kusintha khalidwe lake.—Akol. 3:8-10.