Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Ine Ndilipo! Nditumizeni”

“Ine Ndilipo! Nditumizeni”

Tonsefe tiyenera kutsanzira Yesaya pokhala ndi mtima wodzipereka. Iye anasonyeza chikhulupiriro ndipo anavomera mwamsanga kutumidwa ngakhale kuti sankadziwa zambiri zokhudza ntchito imene agwire. (Yes. 6:8) Kodi inuyo mungasinthe zinthu zina pa moyo wanu kuti mukatumikire kudera limene kukufunika olalikira Ufumu ambiri? (Sal. 110:3) N’zoona kuti muyenera “kuwerengera” mtengo wake musanasankhe kusamuka. (Luka 14:27, 28) Komabe ndi bwino kukhala ofunitsitsa kusiya zinthu zina kuti muwonjezere zimene mumachita pa ntchito yolalikira. (Mat. 8:20; Maliko 10:28-30) Vidiyo yakuti Kusamukira Kumene Kukufunika Olalikira Ambiri, imasonyeza kuti madalitso amene timapeza potumikira Yehova amakhala ambiri kuposa zinthu zimene tingasiye.

MUKAONERA VIDIYOYI, YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi anthu a m’banja la a Williams analolera kusiya komanso kusintha zinthu ziti kuti akatumikire ku Ecuador?

  • Kodi anaganizira zinthu ziti posankha dziko loti akatumikire?

  • Kodi anapeza madalitso otani?

  • Kodi mungapeze kuti mfundo zokuthandizani ngati mukufuna kusamukira kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri?

PA KULAMBIRA KWANU KWA PABANJA, KAMBIRANANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi banja lathu lingawonjezere bwanji zimene timachita potumikira Yehova? (km 8/11 4-6)

  • Ngati sitingathe kusamukira kudera lina, kodi tingawonjezere bwanji zimene timachita pothandiza mpingo wathu? (w16.03 23-25)