Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu  |  December 2016

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizifika Anthu Pamtima ndi Buku Lakuti Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?

Tizifika Anthu Pamtima ndi Buku Lakuti Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?

KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Kuti anthu azilambira Yehova m’njira yovomerezeka, ayenera kuphunzira mfundo za m’Baibulo n’kumazitsatira pa moyo wawo. (Yes. 2:3, 4) Buku la ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’ ndi buku lachiwiri limene timaphunzira ndi anthu ndipo limathandiza munthu kudziwa mmene angagwiritsire ntchito mfundo za Mulungu. (Aheb. 5:14) Tikamaphunzitsa anthu tiyenera kuyesetsa kuwafika pamtima n’cholinga choti azitha kusintha zinthu pa moyo wawo.—Aroma 6:17.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Muzikonzekera mokwanira n’kumaganizira mfundo zomwe zingamuthandize munthuyo. Muzimufunsa mafunso amene angamuchititse kufotokoza maganizo ake pa zimene mukukambirana.—Miy. 20:5; be 259

  • Muzigwiritsa ntchito mabokosi omwe ali m’bukuli kuti munthuyo aziona ubwino wotsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wake

  • Pa nkhani zimene munthu ayenera kutsatira chikumbumtima chake, muzimuthandiza kuganizira mfundo zofunika, koma musamamusankhire zochita.—Agal. 6:5

  • Yesetsani kudziwa ngati wophunzira wanu akufunikira kumuthandiza kuti azitsatira mfundo zina za m’Baibulo. Koma muzikhala wosamala pochita zimenezi. Muzimulimbikitsa mokoma mtima kuti azitsatira mfundo za m’Baibulo chifukwa chokonda Yehova.—Miy. 27:11; Yoh. 14:31