Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzicheza ndi Anthu Amene Amakonda Yehova

Muzicheza ndi Anthu Amene Amakonda Yehova

N’chifukwa chiyani tiyenera kumacheza ndi anthu amene amakonda Yehova? Chifukwa chake ndi choti anthu amene timacheza nawo angachititse kuti tikhale ndi makhalidwe abwino kapena oipa. (Miy. 13:20) Mwachitsanzo, Mfumu Yehoasi inkachita “zoyenera pamaso pa Yehova” chifukwa chokonda kucheza ndi Yehoyada yemwe anali mkulu wa ansembe. (2 Mbiri 24:2) Koma Yehoyada atangomwalira, Yehoasi anayamba kuchita zoipa chifukwa chocheza ndi anthu oipa.​—2 Mbiri 24:17-19.

M’nthawi ya atumwi, Paulo anayerekezera mpingo wachikhristu ndi ‘nyumba yaikulu’ ndipo anthu a mumpingo anawayerekezera ndi “ziwiya,” kapena kuti zipangizo zogwiritsa ntchito pakhomo. Timakhalabe “chiwiya cha ntchito yolemekezeka” tikamapewa kucheza ndi aliyense amene amachita zinthu zimene Yehova amadana nazo ngakhale atakhala wa m’banja lathu kapena wa mumpingo wathu. (2 Tim. 2:20, 21) Choncho, tiyeni tizicheza ndi anthu amene amakonda Yehova komanso amene amatilimbikitsa kuti tizimutumikira.

ONERANI VIDIYO YAKUTI, MUZIPEWA KUGWIRIZANA NDI ANTHU A MAKHALIDWE OIPA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi tingayambe bwanji kucheza ndi anthu oipa?

  • N’chiyani chomwe chinathandiza Akhristu atatu m’vidiyoyi kuti asiye kugwirizana ndi anthu oipa?

  • Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zomwe zingakuthandizeni kusankha mwanzeru anthu ocheza nawo?

Kodi ndine “chiwiya cha ntchito yolemekezeka”?​—2 Tim. 2:21