Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 4-6

Yesetsani Kuti Mulowe Mumpumulo wa Mulungu

Yesetsani Kuti Mulowe Mumpumulo wa Mulungu

4:11

Tikhoza kulowa mumpumulo wa Yehova tikamayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga chake chomwe amatiuza kudzera m’gulu lake. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimachita zotani ndikapatsidwa uphungu? Kodi ndimatani pakakhala kusintha pa nkhani ya mmene timamvera Malemba?’

Kodi ndi mayesero ati omwe angachititse kuti ndisamvere Yehova?