Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ofalitsa akugawira kabuku ka Uthenga Wabwino ku Azerbaijan

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU August 2017

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za Ulaliki wa Galamukani! ndiponso kuphunzitsa choonadi pa nkhani yokhudza chifukwa chimene Mulungu analengera anthu. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mupange ulaliki wanuwanu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yehova Anapereka Cholowa kwa Anthu Omwe Sankamulambira

Yehova anapereka cholowa kwa Ababulo atazinga mzinda wa Turo kwa zaka 13. Ndiye kodi sangayamikire ntchito imene atumiki ake okhulupirika amagwira komanso nsembe zimene amapereka?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzikhala ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo​—Kudzichepetsa

N’chifukwa chiyani kudzichepetsa n’kofunika? Kodi tingasonyeze bwanji kudzichepetsa? Kodi pemphero komanso chitsanzo cha Yesu zingatithandize bwanji kuti tikhale odzichepetsa?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Udindo Waukulu wa Mlonda

Mlonda anali ndi udindo wochenjeza anthu ngati kukubwera zoopsa. Kodi Yehova ankatanthauza chiyani pamene mophiphiritsira anasankha Ezekieli kuti akhale mlonda wa nyumba ya Isiraeli?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzikhala ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo​—Kulimba Mtima

N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa anthu? Kodi kusinkhasinkha, kupemphera komanso kukhulupirira Yehova kungatithandize bwanji kukhala olimba mtima?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Gogi wa ku Magogi Awonongedwa Posachedwapa

Baibulo limafotokoza zimene zidzachitike Gogi wa ku Magogi asanawonongedwe komanso akadzawonongedwa.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzikhala ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo​—Chikhulupiriro

Mofanana ndi Abrahamu, ifenso tizikhulupirira Yehova ngakhale pamene kuchita zimenezi kuli kovuta. Kodi tingatani kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Mmene Masomphenya a Ezekieli Onena za Kachisi Akutikhudzira

Masomphenya a Ezekieli onena za Kachisi amatithandiza kudziwa kuti Yehova ali ndi mfundo zapamwamba za makhalidwe abwino zokhudza kulambira koyera. Kodi masomphenyawa angatithandize bwanji?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Ndingadzachitenso Liti Upainiya Wothandiza?

Njira imodzi imene tingaperekere nsembe zotamanda ndi kuchita upainiya wothandiza. Kodi mungasinthe zinthu zina kuti muchite utumikiwu?