GALAMUKANI!

Funso: Kodi mukuganiza kuti zinthu zingakhale bwino padzikoli ngati anthu onse atasiya zoipa zimene anazolowera kuchita n’kumayesetsa kuchita zabwino?

Lemba: Mlal. 7:8a

Perekani Magaziniyo: Nkhani za m’magaziniyi zikufotokoza mfundo za m’Baibulo zomwe zingathandize anthu kuti azikonda kuchita zinthu zabwino.

GALAMUKANI!

Funso: Nthawi zina zinthu zingasinthe mosayembekezereka pa moyo wathu ndipo palibe zomwe tingachite kuti zimenezi zisachitike. Kodi mukuganiza kuti munthu angatani ngati zinthu zasintha pa moyo wake?

Lemba: Mlal. 7:10

Perekani magaziniyo: [Musonyezeni nkhani imene ikuyambira patsamba 10.] Nkhaniyi ikufotokoza mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize zinthu zikasintha pa moyo wathu.

MVERANI MULUNGU KUTI MUDZAPEZE MOYO WOSATHA

Funso: Aliyense, kuphatikizapo achibale komanso anzathu, ali ndi dzina. Koma nanga bwanji Mulungu, kodi nayenso ali ndi dzina? Nanga dzina lake ndi ndani?

Lemba: Sal. 83:18

Perekani Kabukuko: Kabuku aka kakufotokoza zinthu zinanso zomwe Baibulo limanena zokhudza Mulungu. [Musonyezeni tsamba 6 ndi 7.]

LEMBANI NJIRA INA IMENE MUNGAGWIRITSE NTCHITO

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.